Maliro 2

Yerusalemu amangidwa misasa, njala isautsa, mudzi upasuka

1 Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira!

Wagwetsa pansi kucokera kumwamba kukoma kwace kwa Israyeli;

Osakumbukira poponda mapazi ace tsiku la mkwiyo wace.

2 Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazicitira cisoni;

Wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wace;

Wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ace.

3 Pokwiya moopsya walikha nyanga zonse za Israyeli;

Wabweza m’mbuyo dzanja lace lamanja pamaso pa adaniwo,

Natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.

4 Wathifula uta wace ngati mdani, waima ndi dzanja lace lamanja ngati mmaliwongo;

Wapha onse okondweretsa maso;

Watsanulira ukali wace ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.

5 Yehova wasanduka mdani, wameza Israyeli;

Wameza zinyumba zace zonse, wapasula malinga ace;

Nacurukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi cibumo.

6 Wacotsa mwamphamvu dindiro lace ngati la m’munda;

Waononga mosonkhanira mwace;

Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi sabata m’Ziyoni;

Wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.

7 Ambuye wataya guwa lace la nsembe, malo ace opatulika amnyansira;

Wapereka m’manja a adani ace makoma a zinyumba zace;

Iwo anaphokosera m’nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.

8 Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni;

Watambalika cingwe, osabweza dzanja lace kuti lisaonongepo;

Waliritsa chemba ndi linga; zilefuka pamodzi.

9 Zipata zace zalowa pansi; waononga ndi kutyola mipiringidzo yace;

Mfumu yace ndi akalonga ace ali pakati pa amitundu akusowa cilamulo;

Inde, aneneri ace samalandira masomphenya kwa Yehova.

10 Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;

Aponya pfumbi pa mitu yao, namangirira ciguduli m’cuuno mwao:

Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.

11 Maso anga alefuka ndi misozi, m’kati mwanga mugwedezeka;

Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga;

Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m’makwalala a mudziwu.

12 Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?

Pokomoka iwo ngati olasidwa m’makwalala a mudziwu,

Potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.

13 Ndikucitire umboni wotani? ndikuyerekeze ndi ciani, mwana wamkazi wa Yerusalemu?

Ndikulinganize ndi ciani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?

Popeza akula ngati nyanja; ndani angakucize?

14 Aneneri ako anakuonera masomphenya acabe ndi opusa;

Osaulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,

Koma anakuonera manenero acabe ndi opambutsa.

15 Onse opita panjira akuombera manja:

Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,

Kodi uwu ndi mudzi wochedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?

16 Adani ako onse ayasamira pa iwe, Atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza;

Ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.

17 Yehova wacita comwe analingalira;

Watsiriza mau ace, amene analamulira nthawi yakale;

Wagwetsa osacitira cisoni;

Wakondweretsa adani pa iwe,

Wakweza nyanga ya amaliwongo ako.

18 Mtima wao unapfuula kwa Ambuye,

Linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku;

Usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.

19 Tauka, tapfuula usiku, poyamba kulonda;

Tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye;

Takwezera maso ako kwa Iye, cifukwa ca moyo wa tiana tako,

Timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.

20 Onani Yehova, nimupenye, mwacitira ayani ici?

Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawaseweza?

Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m’malo opatulika a Ambuye?

21 Wamng’ono ndi nkhalamba agona pansi m’makwalala;

Anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga;

Munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osacitira cisoni.

22 Mwaitana zondiopsya mozungulira ngati tsiku la msonkhano;

Panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova;

Omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.