Ezekieli 2

Kuitanidwa kwa Ezekieli

1 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, khala ciriri, ndipo ndidzanena nawe.

2 Ndipo unandilowa mzimu pamene ananena nane, ndi kundiimika ndikhale ciriri; ndipo ndinamumva Iye wakunena nane.

3 Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israyeli, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe.

4 Ndipo anawa, ndiwo acipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nao, Atero Yehova Mulungu.

5 Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.

6 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka.

7 Ndipo ukanene nao mau anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka.

8 Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ici ndirikunena nawe; usakhale iwewopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye comwe ndikupatsa.

9 Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londiturutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m’mwemo;

10 naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m’kati ndi kubwalo; munalembedwa m’mwemo nyimbo za maliro, ndi cisoni, ndi tsoka.