Ezekieli 15

Mtengo wopanda pace

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uli wonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango?

3 Kodi atengako mtengo kupanga nao nchito? atengako ciciri kodi kupacikapo cipangizo ciri conse?

4 Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zace zonse ziwiri, nupserera pakati pace, kodi ukomera nchito Irf yonse?

5 Taonani, pokhala wamphumphu sunayenera nchito iri yonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso nchito iri yonse?

6 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala m’Yerusalemu.

7 Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzaturuka kumoto, koma moto udzawatha; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.

8 Ndipo ndidzasandutsa dziko cipululu; popeza anacita colakwa, ati Ambuye Yehova.