Hoseya 6

Israyeli abwerera kunka kwa Yehova

1 Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang’amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.

2 Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lacitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pace.

3 Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kuturuka kwace kwakonzekeratu ngati matanda kuca; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.

Efraimu ndi Yuda adrudzulidwa

4 Efraimu iwe, ndidzakucitira ciani? Yuda iwe, ndikucitire ciani? pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam’mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.

5 Cifukwa cace ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga aturuka ngati kuunika.

6 Pakuti ndikondwera naco cifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu koposa nsembe zopsereza.

7 Koma iwo analakwira cipangano ngati Adamu, m’mene anandicitira monyenga.

8 Gileadi ndiwo mudzi wa ocita zoipa, wa mapazi a mwazi.

9 Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi acita coipitsitsa.

10 M’nyumba ya Israyeli ndinaona cinthu coopsetsa; pamenepo pali citole ca Efraimu; Israyeli wadetsedwa.

11 Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.