Elifazi adzudzula Yobu; tsoka la munthu licokera ku zoipa zace; Yobu alape
1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2 Munthu akayesa kunena nawe mau, kodi udzamva nao cisoni?
Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?
3 Taona iwe walangiza aunyinji,
Walimbitsa manja a ofoka.
4 Mau ako anacirikiza iye amene akadagwa,
Walimbitsanso maondo otewa.
5 Koma tsopano cakufikira iwe, ndipo ukomoka;
Cikukhudza, ndipo ubvutika.
6 Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,
Ndi ciyembekezo cako si ndiwo ungwiro wa njira zako?
7 Takumbukila tsopano, watayika ndani wosaparamula konse?
Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?
8 Monga umo ndaonera, olimira mphulupulu,
Nabzala bvuto, akololapo zomwezo.
9 Atayika ndi mpweya wa Mulungu,
Nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wace.
10 Kubangula kwa mkango, ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,
Ndi mano a misona ya mkango atyoledwa.
11 Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,
Ndi misona ya mkango waukazi imwazika.
12 Anditengera mau m’tseri,
M’khutu mwanga ndinalandira kunong’oneza kwace.
13 M’malingaliro a masomphenya a usiku,
Powagwira anthu tulo tatikuru,
14 Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,
Nanthunthumira nako mafupa anga onse.
15 Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;
Tsitsi la thupi langa lidati nyau nyau.
16 Unaima ciriri, koma sindinatha kuzindikira maonekedwe ace;
Panali mzukwa pamaso panga;
Kunali cete, ndipo ndidamva mau akuti,
17 Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?
Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wace?
18 Taona, sakhulupirira atumiki ace;
Nawanenera amithenga ace zopusa;
19 Kopambana kotani nanga iwo akukhala m’nyumba zadothi,
Amene kuzika kwao kuti m’pfumbi,
Angothudzulidwa ngati gulugufe,
20 Kuyambira m’mawa kufikira madzulo athudzuka;
Aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.
21 Kukometsetsa kwao sikumacotsedwa nao?
Amafa koma opanda nzeru.