Yobu abwereza kukana kuti sanacimwa. Mulungu wosadziwika acita cifuniro cace. Kwambiri ocimwa oyenera kulangidwa akhala bwino m’moyo uno
1 Koma Yobu anayankha, nati,
2 Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;
Kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m’kulemera kwace.
3 Ha! ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,
Kuti ndifike ku mpando wace!
4 Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pace,
Ndikadadzaza m’kamwa mwanga ndi matsutsano.
5 Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,
Ndikadazindikira cimene akadanena nane.
6 Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yace yaikuru?
Iai, koma akadandicherera khutu.
7 Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;
Ndipo ndikadapulumuka cipulumukire kwa Woweruza wanga.
8 Taonani, ndikamka m’tsogolo, kulibe Iye;
Kapena m’mbuyo sindimzindikira;
9 Akacita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;
Akabisala kulamanja, sindimuona,
10 Koma adziwa njira ndilowayi;
Atandiyesa ndidzaturuka ngati golidi.
11 Phazi langa lagwiratu moponda Iye,
Ndasunga njira yace, wosapambukamo.
12 Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yace;
Ndasungitsa mau a pakamwa pace koposa lamulo langa langa.
13 Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?
Ndi ici cimene moyo wace ucifuna acicita.
14 Pakuti adzacita condiikidwiratu;
Ndipo zambiri zotere ziri ndi Iye.
15 Cifukwa cace ndiopsedwa pankhope pace;
Ndikalingirira, ndicita mantha ndi Iye.
16 Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,
Ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.
17 Popeza sindinalikhidwa usanafike mdimawo,
Ndipo sanandiphimbira nkhope yanga ndi mdima wa bii.