Kusiyana pakati pa olungama ndi oipa
1 WODALA munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa,
Kapena wosaimirira m’njira ya ocimwa,
Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.
2 Komatu m’cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace;
Ndipo m’cilamulo cace amalingima usana ndi usiku.
3 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi;
Wakupatsa cipatso cace pa nyengo yace,
Tsamba lace lomwe losafota;
Ndipo zonse azicita apindula nazo.
4 Oipa satero ai;
Koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.
5 Cifukwa cace oipa sadzaimirira pa mlanduwo,
Kapena ocimwa mu msonkhano wa olungama.
6 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama;
Koma mayendedwe a oipa adzatayika.