Ufumu wa wodzozedwa wa Yehova
1 Aphokoseranji amitundu.
Nalingiriranji anthu zopanda pace?
2 Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi,
Nacita upo akulu pamodzi,
Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wace, ndi kuti.
3 Tidule zomangira zao,
Titaye nsinga zao.
4 Wokhala m’mwambayo adzaseka;
Ambuye adzawanyoza.
5 Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wace,
Nadzawaopsa m’ukali wace:
6 Koma Ine ndadzoza mfumu yanga
Pa Ziyoni, phiri langa loyera.
7 Ndidzauza za citsimikizo:
Yehova ananena ndi
Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga;
Ine lero ndakubala.
8 Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale colowa cako,
Ndi malekezero a dziko lapansi akhale ako ako.
9 Udzawatyola ndi ndodo yacitsulo;
Udzawaphwanya monga mbiya yawoumba.
10 Tsono, mafumu inu, citani mwanzeru:
Langikani, oweruza inu a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova ndi mantha,
Ndipo kondwerani ndi cinthenthe.
12 Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m’njira,
Ukayaka pang’ono pokha mkwiyo wace.
Odala onse akumkhulupirira Iye.