Pemphero posautsidwa
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Nesmoto. Salmo la Davide.
1 Pakupfuula ine mundiyankhe, Mulungu wa cilungamo canga;
Pondicepera mwandikulitsira malo:
Ndicitireni cifundo, imvani pemphero langa.
2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?
Mudzakonda zacabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?
3 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo
Adzamva Yehova m’mene ndimpfuulira Iye,
4 Citani cinthenthe, ndipo musacimwe:
Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale cete.
5 Iphani nsembe za cilungamo,
Ndipo mumkhulupirire Yehova.
6 Ambiri amati, Adzationetsa cabwino ndani?
Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
7 Mwapatsa cimwemwe mumtima mwanga,
Cakuposa cao m’nyengo yakucuruka dzinthu zao ndi vinyo wao.
8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;
Cifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.