Matsoka a oipa, madalitso a olungama
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Nekiloto. Salimo la Davide.
1 Mverani mau anga, Yehova,
Zindikirani kulingirira kwanga.
2 Tamvetsani mau a kupfuula kwanga,
Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga:
Pakuti kwa Inu ndimapemphera,
3 M’mawa, Yehova, mudzamva mau anga;
M’mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
4 Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera naco coipa
Mphulupulu siikhala ndi Inu.
5 Opusa sadzakhazikika pamaso panu:
Mudana nao onse akucita zopanda pace.
6 Mudzaononga iwo akunena bodza:
Munthu wokhetsa mwazi ndi wacinyengo, Yehova anyansidwa naye.
7 Koma ine, mwa kucuruka kwa cifundo canu ndidzalowa m’nyumba yanu:
Ndidzagwada kuyang’ana Kacisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
8 Yehova, munditsogolere m’cilungamo canu, cifukwa ca akundizondawo;
Mulungamitse njira yanu pamaso panga.
9 Pakuti m’kamwa mwao mulibe mau okhazikika;
M’kati mwao m’mosakaza;
M’mero mwao ndi manda apululu:
Lilime lao asyasyalika nalo.
10 Muwayese otsutsika Mulungu;
Agwe nao uphungu wao:
M’kucuruka kwa zolakwa zao muwapitikitse;
Pakuti anapikisana ndi Inu.
11 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,
Apfuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;
Nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.
12 Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;
Mudzamcinjiriza naco cibvomerezo ngati cikopa.