Yehova asunga anthu ace nalanga oipa
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salmo la Davide.
1 Ndakhulupirira Yehova:
Mutani nkunena kwa moyo wanga,
Thawirani ku phiri lanu ngati mbalame?
2 Pakuti, onani, oipa akoka uta,
Apiringidza mubvi wao pansinga,
Kuwaponyera mumdima oongoka mtima.
3 Akapasuka maziko,
Wolungama angacitenji?
4 Yehova ali m’Kacisi wace woyera,
Yehova, mpando wacifumu wace uli m’Mwamba;
Apenyerera ndi maso ace, ayesa ana a anthu ndi zikope zace.
5 Yehova ayesa wolungama mtima:
Koma moyo wace umuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa.
6 Adzagwetsa pwata pwata misampha pa oipa;
Moto ndi miyala yasuifure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m’cikho cao.
7 Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama:
Woongoka mtima adzapenya nkhope yace.