Anthu ndi amabodza, Mulungu ndiye woona
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Seminiti
1 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;
Pakuti okhulupirika acepa mwa ana a anthu.
2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wace:
Amanena ndi mlomo wotyasika, ndi mitima iwiri.
3 Yehova adzadula milomo yonse yotyasika,
Lilime lakudzitamandira:
4 Amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;
Milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?
5 Cifukwa ca kupasuka kwa ozunzika, cifukwa ca kuusa moyo kwa aumphawi,
Ndiuka tsopano, ati Yehova; Ndidzamlonga mosungika muja alaka-lakamo.
6 Mau a Yehova ndi mau oona;
Ngati siliva woyenga m’ng’anjo yadothi,
Yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.
7 Mudzawasunga, Yehova,
Mudzawacinjirizira mbadwo uno ku nthawi zonse.
8 Oipa amayenda mozungulira-zungulira,
Potamanda iwo conyansa mwa ana a anthu.