Anthu oipadi
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salmo la Davide.
1 Waucitsiru amati mumtima mwace, Kulibe Mulungu.
Acita zobvunda, acita nchito zonyansa;
Kulibe wakucita bwino.
2 Yehova m’Mwamba anaweramira pa ana a anthu,
Kuti aone ngati aliko wanzeru,
Wakufuna Mulungu.
3 Anapatuka onse; pamodzi anabvunda mtima;
Palibe wakucita bwino ndi mmodzi yense.
4 Kodi onse ocita zopanda pace sadziwa kanthu?
Pakudya anthu anga monga akudya mkate,
Ndipo saitana pa Yehova.
5 Pamenepa anaopa-opatu:
Pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.
6 Munyazitsa uphungu wa wozunzika,
Koma Yehova ndiye pothawira pace.
7 Mwenzi cipulumutso ca Israyeli citacokera ku Ziyoni!
Pakubweretsa Yehova anthu ace a m’nsinga,
Pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israyeli.