Munthu wokhulupira Mulungu akhazikika mtima, osaopa kutayika
Mlkitamu wa Davide.
1 Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.
2 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga:
Ndiribe cabwino cina coposa Inu.
3 Za oyera mtima okhala pa dziko lapansi,
Iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli cikondwero canga conse.
4 Zidzacuruka zisoni zao za iwo otsata mulungu wina:
Sindidzathira nsembe zao zamwazi,
Ndipo sindidzachula maina ao pakamwa panga,
5 Yehova ndiye gawo la colowa canga ndi cikho canga:
Ndinu wondigwirira colandira canga,
6 Zingwe zandigwera mondikondweretsa;
Inde cosiyira cokoma ndiri naco.
7 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandicitira uphungu:
Usikunso imso zanga zindilangiza.
8 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse:
Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
9 Cifukwa cace wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga;
Mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
10 Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;
Simudzalola wokondedwa wanu abvunde.
11 Mudzandidziwitsa njira ya moyo:
Pankhope panu pali cimwemwe cokwanira;
M’dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.