Davide alemekeza zolengedwa ndi Mulungu, ndi malamulo ao omwe
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davide
1 Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu;
Ndipo thambo lionetsa nchito ya manja ace.
2 Usana ndi usana ucurukitsa mau,
Ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.
3 Palibe cilankhulidwe, palibe mau;
Liu lao silimveka.
4 Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi,
Ndipo mau ao ku malekezero a m’dziko muli anthu.
Iye anaika hema la dzuwa m’menemo,
5 Ndipo liri ngati mkwati wakuturuka m’cipinda mwace,
Likondwera ngati ciphona kuthamanga m’njira.
6 Kuturuka kwace lituruka kolekezera thambo,
Ndipo kuzungulira kwace lifikira ku malekezero ace:
Ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwace.
7 Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;
Mboni za Yehova ziri zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru;
8 Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima:
Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
9 Kuopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthawi zonse:
Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konse konse.
10 Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa:
Zizuna koposa uci ndi zakukha za zisa zace,
11 Ndiponso kapolo wanu acenjezedwa nazo:
M’kuzisunga izo muli mphotho yaikuru.
12 Adziwitsa zolowereza zace ndani?
Mundimasule kwa zolakwa zobisika.
13 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;
Zisacite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro,
Ndi wosacimwa colakwa cacikuru.
14 Mau a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga abvomerezeke pamaso panu,
Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga,