Davide ayamika Mulungu pa kugonjetsa adani
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide,
1 Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;
Adzakondwera kwakukuru m’cipulumutso canu!
2 Mwampatsa iye cikhumbo ca mtimawace,
Ndipo simunakana pempho la milomo yace.
3 Pakuti mumkumika iye ndi madalitso okoma:
Muika korona wa golidi woyengetsa pamutu pace.
4 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;
Mwamtalikitsira masiku ku nthawi za nthawi.
5 Ulemerero wace ngwaukuru mwa cipulumutso canu:
Mumcitira iye ulemu ndi ukulu.
6 Pakuti mumuikira madalitso ku nthawi zonse;
Mumkondweretsa ndi cimwemwe pankhope panu.
7 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,
Ndipo mwa cifundo ca Wam’mwambamwamba sadzagwedezeka iye,
8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse:
Dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.
9 Mudzawaika ngati ng’anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.
Yehova adzawatha m’kukwiya kwace,
Ndipo moto udzawanyeketsa.
10 Mudzaziononga zobala zao kuzicotsa pa dziko lapansi,
Ndi mbeu zao mwa ana a anthu.
11 Pakuti anakupangirani coipa:
Anapangana ciwembu, osakhoza kucicita.
12 Pakuti mudzawabweza m’mbuyo,
Popiringidza m’nsinga zanu pankhope pao,
13 Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu:
Potero tidzayimba ndi kulemekeza cilimbiko canu.