Posautsidwa Davide adandaulira, apemphera, ayamika Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Ajelet Hasakara, Salmo la Davide.
1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?
Mukhaliranji kutali kwa cipulumutso canga, ndi kwa mau a kubuula kwanga?
2 Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simubvomereza;
Ndipo usiku, sindikhala cete.
3 Koma Inu ndinu woyera,
Wakukhala m’malemekezo a Israyeli.
4 Makolo athu anakhulupirira Inu:
Anakhulupirira, ndipo munawalanditsa.
5 Anapfuula kwa Inu, napulumutsidwa:
Anakhulupita Inu, ndipo sanacita manyazi.
6 Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai:
Cotonza ca anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.
7 Onse akundipenya andiseka:
Akwenzula, apukusa mutu, nati,
8 Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa,
Amlanditse tsopano popeza akondwera naye.
9 Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa:
Wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.
10 Cibadwire ine anandisiyira Inu:
Kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.
11 Musandikhalire kutali; pakuti nsautso iri pafupi:
Pakuti palibe mthandizi.
12 Ng’ombe zamphongo zambiri zandizinga:
Mphongo zolimba za ku Basana zandizungulira,
13 Andiyasamira m’kamwa mwao,
Ngati mkango wozomola ndi wobangula.
14 Ndathiridwa pansi monga madzi,
Ndipo mafupa anga onse anaguluka:
Mtima wanga ukunga sera; Wasungunuka m’kati mwa matumbo anga,
15 Mphamvu yanga yauma ngati phale;
Ndi lilime langa likangamira ku nsaya zanga;
Ndipo mwandifikitsa ku pfumbi la imfa.
16 Pakuti andizinga agaru:
Msonkhano wa oipa wanditsekereza;
Andiboola m’manja anga ndi m’mapazi anga.
17 Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse;
Iwo ayang’ana nandipenyetsetsa ine:
18 Agawana zobvala zanga,
Nalota maere pa malaya anga,
19 Koma Inu, Yehova, musakhale kutari;
Mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza.
20 Landitsani moyo wanga kulupanga;
Wokondedwa wanga ku mphamvu ya garu,
21 Ndipulumutseni m’kamwa mwa mkango;
Inde mwandiyankha ine ndiri pa nyanga za njati,
22 Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga:
Pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.
23 Inu akuopa Yehova, mumlemekeze;
Inu nonse mbumba ya Yakobo, mumcitire ulemu;
Ndipo mucite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israyeli.
24 Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika;
Ndipo sanambisira nkhope yace;
Koma pompfuulira Iye, anamva.
25 Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukuru:
Zowinda zanga ndidzazicita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
26 Ozunzika adzadya nadzakhuta:
Adzayamika Yehova iwo amene amfuna:
Ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.
27 Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukila nadzatembenukira kwa Yehova:
Ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.
28 Pakuti ufumuwo ngwa Yehova;
Iye acita ufumu mwa amitundu.
29 Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira:
Onse akutsikira kupfumbi adzawerama pamaso pace,
Ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wace.
30 Mbumba ya anthu idzamtumikira;
Kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.
31 Iwo adzadza nadzafotokozera cilungamo cace
Kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anacicita.