Ulemerero wa Yehova
Salmo la Davide,
1 Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zace zomwe,
Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m’mwemo.
2 Pakuti Iye analimanga pazinyanja,
Nalikhazika pamadzi.
3 Adzakwera ndani m’phiri la Yehova?
Nadzaima m’malo ace oyera ndani?
4 Woyera m’manja, ndi woona m’mtima, ndiye;
Iye amene sanakweza moyo wace kutsata zacabe,
Ndipo salumbira monyenga,
5 Iye adzalandira dalitso kwa Yehova,
Ndi cilungamo kwa Mulungu wa cipulumutso cace.
6 Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye,
Iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.
7 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;
Ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha:
Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
8 Mfumu imene ya ulemerero ndani?
Yehova wamphamvu ndi wolimba,
Yehova wolimba kunkhondo.
9 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;
Inde weramutsani, zitseko zosatha inu,
Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
10 Mfumu imene ya ulemerero ndani?
Yehova wa makamu makamu, Ndiye Mfumu ya ulemerero.