Alemekeza Mulungu wolenga, wosunga zonse
1 Pfuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima:
Oongoka mtima ayenera kulemekeza.
2 Yamikani Yehova ndi zeze:
Myimbireni ndi cisakasa ca zingwe khumi.
3 Mumyimbire Iye Nyimbo yatsopano;
Muyimbe mwaluso kumveketsa mau.
4 Pakuti mau a Yehova ali olunjika;
Ndi nchito zace zonse zikhulupirika.
5 Iye ndiye wakukonda cilungamo ndi ciweruzo:
Dziko lapansi ladzala ndi cifundo ca Yehova.
6 Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova;
Ndipo ndi mpweya wa m’kamwa mwace khamu lao lonse.
7 Amaunjika madzi a m’nyanja monga mulu:
Amakundika zakudya mosungiramo.
8 Dziko lonse lapansi liope Yehova:
Ponse pali anthu acite mantha cifukwa ca Iye,
9 Pakuti ananena, ndipo cinacitidwa;
Analamulira, ndipo cinakhazikika.
10 Yehova aphwanya upo wa amitundu:
Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.
11 Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire,
Zolingirira za m’mtima mwace ku mibadwo mibadwo.
12 Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao;
Mtundu womwe anausankha ukhale colandira ca iye yekha.
13 Yehova apenyerera m’mwamba; Aona ana onse a anthu.
14 M’malo akhalamo Iye, amapenya pansi
Pa onse akukhala m’dziko lapansi;
15 Iye amene akonza mitima ya iwo onse,
Amene azindikira zocita zao zonse.
16 Palibe mfumu yoti gulu lalikuru limpulumutsa:
Mphamvu yaikuru siicilanditsa ciphona,
17 Kavalo safikana kupulumuka naye:
Cinkana mphamvu yace njaikuru sapulumutsa.
18 Taonani, diso la Yehova liri pa iwo akumuopa Iye,
Pa iwo akuyembekeza cifundo cace;
19 Kupulumutsa moyo wao kwa imfa,
Ndi kuwasunga ndi moyo m’nyengo ya njala.
20 Moyo wathu walindira Yehova:
Iye ndiye thandizo lathu ndi cikopa cathu.
21 Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye,
Cifukwa takhulupirira dzina lace loyera.
22 Yehova, cifundo canu cikhale pa ife,
Monga takuyembekezani Inu.