Kusangalala kwa ocimwa kudzatha, olungama akhalitsa nathandizidwa ndi Mulungu
Salmo la Davide.
1 Usabvutike mtima cifukwa ca ocita zoipa,
Usacite nsanje cifukwa ca ocita cosalungama.
2 Pakuti adzawamweta msanga monga udzu,
Ndipo adzafota monga msipu wauwisi.
3 Khulupirira Yehova, ndipo cita cokoma;
Khala m’dziko, ndipo tsata coonadi.
4 Udzikondweretsenso mwa Yehova;
Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.
5 Pereka njira yako kwa Yehova; Khulupiriranso Iye, adzacicita.
6 Ndipo adzaonetsa cilungamo cako monga kuunika,
Ndi kuweruza kwako monga usana.
7 Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye:
Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m’njira yace,
Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.
8 Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo:
Usabvutike mtima ungacite coipa,
9 Pakuti ocita zoipa adzadulidwa:
Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.
10 Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti:
Inde, udzayang’anira mbuto yace, nudzapeza palibe.
11 Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;
Nadzakondwera nao mtendere wocuruka.
12 Woipa apangira ciwembu wolungama,
Namkukutira mano.
13 Ambuye adzamseka:
Popeza apenya kuti tsiku lace likudza.
14 Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;
Alikhe ozunzika ndi aumphawi,
Aphe amene ali oongoka m’njira:
15 Lupanga lao lidzalowa m’mtima mwao momwe,
Ndipo mauta ao adzatyoledwa.
16 Zocepa zace za wolungama zikoma
Koposa kucuruka kwao kwa oipa ambiri.
17 Pakuti manja a oipa adzatyoledwa:
Koma Yehova acirikiza olungama.
18 Yehova adziwa masiku a anthu angwiro:
Ndipo cosiyira cao cidzakhala cosatha.
19 Sadzacita manyazi m’nyengo yoipa:
Ndipo m’masiku a njala adzakhuta.
20 Pakuti oipa adzatayika,
Ndipo adani ace a Yehova adzanga mafuta a ana a nkhosa:
Adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.
21 Woipa akongola, wosabweza:
Koma wolungama acitira cifundo, napereka.
22 Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi;
Koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.
23 Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;
Ndipo akondwera nayo njira yace.
24 Angakhale akagwa, satayikiratu:
Pakuti Yehova agwira dzanja lace.
25 Ndinali mwana ndipo ndakalamba:
Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa,
Kapena mbumba zace zirinkupempha cakudya.
26 Tsiku lonse acitira cifundo, nakongoletsa;
Ndipo mbumba zace zidalitsidwa.
27 Siyana naco coipa, nucite cokoma,
Nukhale nthawi zonse.
28 Pakuti Yehova akonda ciweruzo,
Ndipo sataya okondedwa ace:
Asungika kosatha:
Koma adzadula mbumba za oipa.
29 Olungama adzalandira dziko lapansi,
Nadzakhala momwemo kosatha.
30 Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru,
Ndi lilime lace linena ciweruzo.
31 Malamulo a Mulungu wace ali mumtima mwace;
Pakuyenda pace sadzaterereka.
32 Woipa aunguza wolungama,
Nafuna kumupha.
33 Yehova sadzamsiya m’dzanja lace:
Ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye.
34 Yembekeza Yehova, nusunge njira yace,
Ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko:
Pakudutidwa oipa udzapenya,
35 Ndapenya woipa, alikuopsa,
Natasa monga mtengo wauwisi wanzika.
36 Koma anapita ndipo taona, kwati zi:
Ndipo ndinampwaira osampeza.
37 Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!
Pakuti ku matsiriziro ace a munthuyo kuti mtendere.
38 Koma olakwa adzaonongeka pamodzi:
Matsiriziro a oipa adzadutidwa.
39 Koma cipulumutso ca olungama cidzera kwa Yehova,
Iye ndiye mphamvu yao m’nyengo ya nsautso.
40 Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa:
Awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa,
Cifukwa kuti anamkhulupirira Iye,