Alemekeza cipulumutso ca Mulungu, alalikira poyera cilungamo ca Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davide.
1 Kuyembekeza ndayembekeza Yehova;
Ndipo anandilola, namva kupfuula kwanga.
2 Ndipo anandikweza kunditurutsa m’dzenje la citayiko, ndi m’thope la pacithaphwi;
Nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.
3 Ndipo anapatsa Nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga, cilemekezo ca kwa Mulungu wanga;
Ambiri adzaciona, nadzaopa,
Ndipo adzakhulupirira Yehova.
4 Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika;
Wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.
5 Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazicita nzambiri,
Ndipo zolingirira zanu za pa ife;
Palibe wina wozifotokozera Inu;
Ndikazisimba ndi kuzichula, Zindicurukira kuziwerenga.
6 Nsembe ndi copereka simukondwera nazo;
Mwanditsegula makutu:
Nsembe yopsereza ndi yamacimo simunapempha.
7 Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza;
M’buku mwalembedwa za Ine:
8 Kucita cikondwero canu kundikonda, Mulungu wanga;
Ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga.
9 Ndalalikira cilungamo mu msonkano waukuru;
Onani, sindidzaletsa milomo yanga,
Mudziwa ndinu Yehova.
10 Cilungamo canu sindinacibisa m’kati mwamtima mwanga;
Cikhulupiriko canu ndi cipulumutso canu ndinacinena;
Cifundo canu ndi coonadi canu sindinacibisira msonkhano waukuru.
11 Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu:
Cifundo canu ndi coonadi canu zindisunge cisungire.
12 Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,
Zocimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;
Ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandicokera mtima.
13 Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni:
Fulumirani kudzandithandiza, Yehova.
14 Acite manyazi nadodome
Iwo akulondola moyo wanga kuti auononge:
Abwerere m’mbuyo, nacite manyazi iwo okondwera kundicitira coipa.
15 Apululuke, mobwezera manyazi ao
Amene anena nane, Hede, hede.
16 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu:
Iwo akukonda cipulumutso canu asaleke kunena, Abuke Yehova.
17 Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi;
Koma Ambuye andikumbukila ine:
Inu ndinu mthandizi wanga, ndi mpulumutsi wanga:
Musamacedwa, Mulungu wanga,