Masalmo 43

Davide alira akhale ku Kacisi

1 Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda cifundo:

Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.

2 Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji?

Ndimayenderanji woliralira cifukwa ca kundipsinja mdani?

3 Tumizirani kuunika kwanu ndi coonadi canu zinditsogolere:

Zindifikitse ku phiri lanu loyera,

Kumene mukhala Inuko.

4 Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu,

Kufikira Mulungu wa cimwemwe canga ceniceni:

Ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?

Ndi kuzingwa m’kati mwanga?

Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso,

Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.