Nyimbo voyimbira ukwati wa mfumu
Kwa Mkulu wa Nyimbo pa Syosyanim. Cilangizo ca kwa ana a Kora. Nyimbo ya cikondi.
1 Mtima wanga usefukira naco cinthu cokoma:
Ndinena zopeka ine za mfumu:
Lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.
2 Inu ndinu wokongola ndithu kuposa ana a anthu;
Anakutsanulirani cisomo pa milomo yanu:
Cifukwa cace Mulungu anakudalitsani kosatha.
3 Dzimangireni lupanga lanu m’cuuno mwanu, wamphamvu inu,
Ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.
4 Ndipo pindulani, m’ukulu wanu yendani,
Kaamba ka coonadi ndi cifatso ndi cilungamo:
Ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.
5 Mibvi yanu njakuthwa;
Mitundu ya anthu igwa pansi pa Inu:
Iwalasa mumtima adani a mfumu.
6 Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zamkamuyaya:
Ndodo yacifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.
7 Mukonda cilungamo, ndipo mudana naco coipa:
Cifukwa cace Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu
Ndi mafuta a cikondwerero kuposa anzanu.
8 Zobvala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasya;
M’zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njobvu mwatoruka zoyimba za zingwe zokukondweretsani.
9 Mwa omveka anu muli ana akazi amafumu:
Ku dzanja lamanja lanu aima mkazi wa mfumu wobvala golidi wa ku Ofiri.
10 Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tachera khutu lako;
Uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;
11 Potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako:
Pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.
12 Ndipo mwana wamkazi wa Turo adzafika nayo mphatso;
Acuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.
13 Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m’kati mwa nyumba:
Zobvala zace nza made agolidi.
14 Adzamtsogolera kwa mfumu wabvala zamawanga-mawanga:
Anamwali anzace omtsata adzafika nao kwa inu.
15 Adzawatsogolera ndi cimwemwe ndi kusekerera:
Adzalowa m’nyumba ya mfumu.
16 M’malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako,
Udzawaika akhale mafumu m’dziko lonse lapansi.
17 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m’mibadwo mibadwo:
Cifukwa cace mitundu ya anthu idzayamika Inu ku nthawi za nthawi.