Davide abvomereza kucimwa kwace, apempha Mulungu amkhululukire, asamcotsere Mzimu Woyera
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davide; m’mene anamdzera Natani mnenertso atalowa iye kwa Bateseba.
1 Mundicitire ine cifundo, Mulungu,
Monga mwa kukoma mtima kwanu;
Monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu
Mufafanize macimo anga.
2 Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga,
Ndipo mundiyeretse kundicotsera coipa canga,
3 Cifukwa ndazindikira macimo anga;
Ndipo coipa canga ciri pamaso panga cikhalire:
4 Pa Inu, Inu nokha, ndinacimwa,
Ndipo ndinacicita coipaco pamaso panu:
Kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu,
Mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.
5 Onani, ndinabadwa m’mphulupulu:
Ndipo mai wanga anandilandira m’zoipa.
6 Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m’malo a m’katimo;
Ndipo m’malo a m’tseri mudzandidziwitsa nzeru.
7 Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera;
Munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.
8 Mundimvetse cimwemwe ndi kusekera:
Kuti mafupawo munawatyola akondwere.
9 Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga,
Ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.
10 Mundilengere mtima woyera, Mulungu;
Mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga.
11 Musanditaye kundicotsa pamaso panu;
Musandicotsere Mzimu wanu Woyera.
12 Mundibwezere cimwemwe ca cipulumutso canu;
Ndipo mzimu wakulola undigwirizize.
13 Pomwepo ndidzalangiza ocimwa njira zanu;
Ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.
14 Mundilanditse ku mlandu wa mwazi, Mulungu,
Ndinu Mulungu wa cipulumutso canga;
Lilime langalidzakweza Nyimbo ya cilungamo canu.
15 Ambuye, tsegulani pa milomo yanga;
Ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.
16 Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka;
Nsembe yopsereza simuikonda.
17 Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;
Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.
18 Citirani Ziyoni cokoma monga mwa kukondwera kwanu;
Mumange malinga a miyala a Yerusalemu.
19 Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zacilungamo,
Ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu:
Pamenepo adzapereka
Ng’ombe pa guwa lanu la nsembe.