Davide aneneratu za cionongeko ca oipa, iye nakhulupirira Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Cilangizo ca Davide. Muja analowa Doegi M-edomu nauza Sauli, nati kwa iye, Davide walowa m’nyumba ya Abimeleke.
1 Udzitamandiranji ndi coipa, ciphonaiwe?
Cifundo ca Mulungu cikhala tsiku lonse.
2 Lilime lako likupanga zoipa;
Likunga lumo lakuthwa, lakucita monyenga.
3 Ukonda coipa koposa cokoma;
Ndi bodza koposa kunena cilungamo.
4 Ukonda mau onse akuononga, Lilime lacinyengo, iwe.
5 Potero Mulungu adzakupasula ku nthawi zonse,
Adzakucotsa nadzakukwatula m’hema mwako,
Nadzakuzula, kukucotsa m’dziko la amoyo.
6 Ndipo olungama adzaciona, nadzaopa,
Nadzamseka, ndi kuti,
7 Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyesa Mulungu mphamvu yace;
Amene anatama kucuruka kwa cuma cace,
Nadzilimbitsa m’kuipsa kwace.
8 Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi waazitona m’nyumba ya Mulungu:
Ndikhulupirira cifundo ca Mulungu ku nthawi za nthawi.
9 Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munacicita ici:
Ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ici ncokoma, pamaso pa okondedwa anu,