Masalmo 63

Mtima woliralira kuyanfana ndi Mulungu

Salmo la Davide; muja akakhala m’cipululu ca Yuda.

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m’matanda kuca:

Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu,

M’dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,

Monga ndinakuonani m’malo oyera.

3 Pakuti cifundo canu ciposa moyo makomedwe ace;

Milomo yanga idzakulemekezani.

4 Potero ndidzakuyamikani m’moyo mwanga;

Ndidzakweza manja anga m’dzina lanu.

5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;

Ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakupfuula mokondwera;

6 Pokumbukira Inu pa kama wanga,

Ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7 Pakuti munakhala mthandizi wanga;

Ndipo ndidzapfuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8 Moyo wanga uumirira Inu:

Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,

Adzalowa m’munsi mwace mwa dziko.

10 Adzawapereka ku mphamvu ya lupanga;

Iwo adzakhala gawo la ankhandwe.

11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;

Yense wakulumbirira iye adzatamandira;

Pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.