Davide apempha Mulungu amciniirize pa omlalira
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davido.
1 Imvani Yehova, mau anga, m’kudandaula kwanga;
Sungani moyo wanga angandiopse mdani.
2 Ndibiseni pa upo wacinsinsi wa ocita zoipa;
Pa phokoso la ocita zopanda pace:
3 Amene anola lilime lao ngati lupanga,
Napiringidza mibvi yao, ndiyo mau akuwawitsa;
4 Kuponyera wangwiro mobisika:
Amponyera modzidzimutsa, osaopa.
5 Alimbikitsana m’cinthu coipa;
Apangana za kuchera misampha mobisika;
Akuti, Adzaiona ndani?
6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi kutha;
Cingakhale ca m’kati mwace mwa munthu, ndi mtima wozama.
7 Koma Mulungu adzawaponyera mubvi;
Adzalaswa modzidzimutsa,
8 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;
Onse akuwaona adzawathawa.
9 Ndipo anthu onse adzacita mantha;
Nadzabukitsa cocita Mulungu,
Nadzasamalira nchito yace.
10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye;
Ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.