Davide alemekeza Mulungu pa madalitso ocuruka
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo, nyimbo ya Davide.
1 M’Ziyoni akulemekezani Inu mwacete, Mulungu:
Adzakucitirani Inu cowindaci.
2 Wakumva pemphero Inu,
Zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.
3 Mphulupulu zinandilaka;
Koma mudzafafaniza zolakwa zathu.
4 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,
Akhale m’mabwalo anu:
Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu,
Za m’malo oyera a Kacisi wanu.
5 Mudzatiyankha nazo zoopsa m’cilungamo,
Mulungu wa cipulumutso cathu;
Ndinu cikhulupiriko ca malekezero Onse a dziko lapansi,
Ndi ca iwo okhala kutali kunyanja:
6 Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;
Pozingidwa naco cilimbiko.
7 Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja, kukuntha kwa mafunde ace,
Ndi phokoso la mitundu ya anthu.
8 Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzacita mantha cifukwa ca zizindikilo zanu; Mukondweretsa apo paturukira dzuwa, ndi apo lilowera.
9 Muceza nalo dziko lapansi, muhthirira,
Mulilemeza kwambiri;
Mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi:
Muwameretsera tirigu m’mene munakonzera nthaka.
10 Mukhutitsa nthaka yace yolima;
Mufafaniza nthumbira zace?
Muiolowetsa ndi mbvumbi;
Mudalitsa mmera wace.
11 Mubveka cakaci ndi ukoma wanu;
Ndipo mabande anu akukha zakuca.
12 Akukha pa mabusa a m’cipululu;
Ndipo mapiri azingika naco cimwemwe.
13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;
Ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;
Zipfuula mokondwera, inde ziyimbira.