Amitundu alemekeze Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Neginolo. Salmo, Nyimbo.
1 Aticitire cifundo Mulungu, ndi kutidalitsa,
Atiwalitsire nkhope yace;
2 Kuti njira yanu idziwike pa dziko lapansi,
Cipulumutso canu mwa amitundu onse.
3 Anthu akuyamikeni, Mulungu;
Anthu onse akuyamikeni.
4 Anthu akondwere, napfuule makondwera;
Pakuti mudzaweruza anthu malunjika,
Ndipo mudzalangiza anthu pa dziko lapansi.
5 Anthu akuyamikeni, Mulungu;
Anthu onse akuyamikeni.
6 Dziko lapansi lapereka zipatso zace:
Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.
7 Mulungu adzatidalitsa;
Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye,