Davide apempha Mulungu amlanditse msanga
Kwa Mkulu wa Nyimbo: cikumbutso ca Davtde,
1 Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu;
Fulumirani kundithandiza, Yehova.
2 Acite manyazi, nadodome
Amene afuna moyo wanga:
Abwezedwe m’mbuyo, napepulidwe.
Amene akonda kundicitira coipa,
3 Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao
Amene akuti, Hede, hede.
4 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;
Nanene kosalekeza iwo akukonda cipulumutso canu,
Abuke Mulungu.
5 Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi;
Mundifulumirire, Mulungu:
Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga;
Musacedwe, Yehova.