Za ufumu wa Mfumu yokoma
Salimo la kwa Solomo.
1 Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu,
Ndi mwana wa mfumu cilungamo canu.
2 Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m’cilungamo,
Ndi ozunzika anu ndi m’ciweruzo.
3 Mapiri adzatengera anthu mtendere,
Timapiri tomwe, m’cilungamo.
4 Adzaweruza ozunzika a mwa anthu,
Adzapulumutsa ana aumphawi,
Nadzaphwanya wosautsa.
5 Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi,
Kufikira mibadwo mibadwo.
6 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga:
Monga mvula yothirira dziko.
7 Masiku ace wolungama adzakhazikika;
Ndi mtendere wocuruka, kufikira sipadzakhala mwezi.
8 Ndipo adzacita ufumu kucokera kunyanja kufikira kunyanja,
Ndi kucokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.
9 Okhala m’cipululu adzagwadira pamaso pace;
Ndi adani ace adzaluma nthaka.
10 Mafumu a ku Tarisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera naco copereka;
Mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso,
11 Inde mafumu onse adzamgwadira iye:
Amitundu onse adzamtumikira.
12 Pakuti adzapulumutsa waumphawi wopfuulayo;
Ndi wozunzika amene alibe mthandizi.
13 Adzacitira nsoni wosauka ndi waumphawi,
Nadzapulumutsa moyo wa aumphawi,
14 Adzaombola moyo wao ku cinyengo ndi ciwawa;
Ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pace:
15 Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golidi wa ku Sheba;
Nadzampempherera kosalekeza;
Adzamlemekeza tsiku lonse.
16 M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzocuruka pamwamba pa mapiri;
Zipatso zace zidzati waa, ngati za ku Lebano:
Ndipo iwo a m’mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.
17 Dzina lace lidzakhala kosatha:
Momwe likhalira dzuwa dzina lace lidzamvekera zidzukulu:
Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye;
Amitundu onse adzamucha wodala.
18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli,
Amene acita zodabwiza yekhayo:
19 Ndipo dzina lace la ulemerero lidalitsike kosatha;
Ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wace.
Amen, ndi Amen.
20 Mapemphero a Davide mwana wa Jese atha.