Amitundu apangana kuononga Aisrayeli, Apempha Mulungu awalanditse
Nyimbo. Satmo la Asatu.
1 Mulungu musakhale cete;
Musakhale du, osanena kanthu, Mulungu.
2 Pakuti taonani, adani anu aphokosera:
Ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu,
3 Apangana mocenjerera pa anthu anu,
Nakhalira upo pa obisika anu.
4 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;
Ndipo dzina la Israyeli lisakumbukikenso.
5 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;
Anacita cipangano ca pa Inu:
6 Mahema a Edomu ndi a Aismayeli;
Moabu ndi Ahagara;
7 Gebala ndi Amoni ndi Amaleki;
Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m’Turo.
8 Asuri anaphatikana nao;
Anakhala dzanja la ana a Loti,
9 Muwacitire monga munacitira Midyani;
Ndi Sisera, ndi Jabini ku mtsinje wa Kisoni:
10 Amene anaonongeka ku Endoro;
Anakhala ngati ndowe ya kumunda.
11 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;
Mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna:
12 Amene anati, Tilande
Malo okhalamo Mulungu, akhale athu.
13 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;
Ngati ziputu zomka ndi mphepo.
14 Monga moto upsereza nkhalango,
Ndi monga lawi liyatsa mapiri;
15 Momwemo muwatsate ndi namondwe,
Nimuwaopse ndi kabvumvulu wanu.
16 Acititseni manyazi pankhope pao;
Kuti afune dzina lanu, Yehova.
17 Acite manyazi, naopsedwe kosatha;
Ndipo asokonezeke, naonongeke:
18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,
Ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.