Okhala m’nyumba ya Yehova ndiwo amwai
Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Gitili: Salmo la ana a Kora.
1 Pokhala Inu mpotikonda ndithu, Yehova wa makamu!
2 Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova;
Mtima wanga ndi thupi langa zipfuulira kwa Mulungu wamoyo.
3 Mbawanso inapeza nyumba,
Ndi namzeze cisa cace coikamo ana ace,
Pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu,
Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
4 Odala iwo akugonera m’nyumba mwanu;
Akulemekezani cilemekezere,
5 Wodala munthu amene mphamvu yace iri mwa Inu;
Mumtima mwace muli makwalala a ku Ziyoni,
6 Popyola cigwa ca kulira misozi aciyesa ca akasupe;
Inde mvula: ya cizimalupsa icidzaza ndi madalitso.
7 Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,
Aoneka pamaso pa Mulungu m’Ziyoni.
8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa:
Cherani khutu, Mulungu wa Yakobo.
9 Onani, Mulungu, ndinu cikopa cathu;
Ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.
10 Pakuti tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena,
Kukhala inewapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga,
Kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a coipa,
11 Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi cikopa;
Yehova adzapatsa cifundo ndi ulemerero;
Sadzakaniza cokoma iwo akuyenda angwiro,
12 Yehova wa makamu,
Wodala munthu wakukhulupirira Inu.