Akumbutsa Mulungu madalitso akale, apempha awabwereze
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Satmo la ana a Kora.
1 Munacita zobvomereza dziko lanu, Yehova;
Munabweza ukapolo wa Yakobo.
2 Munacotsa mphulupulu ya anthu anu,
Munafotsera zolakwa zao zonse.
3 Munabweza kuzaza kwanu konse;
Munabwerera ku mkwiyo wanu wotentha.
4 Mutibweze, Mulungu wa cipulumutso cathu,
Nimuletse udani wanu wa pa ife.
5 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?
Kodi mudzakhala cikwiyire mibadwo mibadwo?
6 Kodi simudzatipatsanso moyo,
Kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?
7 Tionetseni cifundo canu, Yehova,
Tipatseni cipulumutso canu.
8 Ndidzamva colankhula Mulungu Yehova;
Pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ace, ndi okondedwa ace;
Koma asabwererenso kucita zapusa.
9 Indedi cipulumutso cace ciri pafupi ndi iwo akumuopa Iye;
Kuti m’dziko mwathu mukhale ulemu.
10 Cifundo ndi coonadi zakomanizana;
Cilungamo ndi mtendere zapsompsonana,
11 Coonadi ciphukira m’dziko;
Ndi cilungamo casuzumira ciri m’mwamba.
12 Inde Yehova adzapereka zokoma;
Ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zace.
13 Cilungamo cidzamtsogolera; Nicidzamkonzera mapazi ace njira.