Anthu onse ayamike Mulungu cifukwa ca nchito zace, cilungamo cace, ndi cifundo cace
Satmo, Nyimbo ya pa Sabata,
1 Nkokoma kuyamika Yehova,
Ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Wam’mwambamwamba Inu:
2 Kuonetsera cifundo canu mamawa,
Ndi cikhulupiriko canu usiku uli wonse.
3 Pa coyimbira ca zingwe khumi ndi pacisakasa;
Pazeze ndi kulira kwace.
4 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kucita kwanu,
Ndidzapfuula mokondwera pa nchito ya manja anu.
5 Ha! nchito zanu nzazikuru, Yehova,
Zolingalira zanu nzozama ndithu.
6 Munthu wopulukira sacidziwa;
Ndi munthu wopusa sacizindikira ici;
7 Cakuti pophuka oipa ngati msipu,
Ndi popindula ocita zopanda pace;
Citero kuti adzaonongeke kosatha:
8 Koma Inu, Yehova, muli m’mwamba ku nthawi yonse.
9 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,
Pakuti, taonani, adani anu adzatayika;
Ocita zopanda pace onse adzamwazika.
10 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;
Anandidzoza mafuta atsopano.
11 Diso langa lapenya cokhumba ine pa iwo ondilalira,
M’makutu mwanga ndamva cokhumba ine pa iwo akucita zoipa akundiukira.
12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;
Adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano.
13 Iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova,
Adzaphuka m’mabwalo a Mulungu wathu.
14 Atakalamba adzapatsanso zipatso;
Adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri:
15 Kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;
Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe cosalungama.