Masalmo 93

Ufumu wa Mulungu ndiwo wa ulemerero, mphamvu, ndi ciyero

1 Yehova acita ufumu; wadzibveka ndi ukulu;

Wadzibveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m’cuuno;

Dziko lomwe lokhalamo anthu likhazikika, silidzagwedezeka.

2 Mpando wacifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija;

Inu ndinu wosayambira ndi kale, lomwe.

3 Mitsinje ikweza, Yehova,

Mitsinje ikweza mkokomo wao;

Mitsinje ikweza mafunde ao.

4 Yehova Wam’mwamba ndiye wamphamvu,

Wakuposa mkokomo wa madzi ambiri,

Ndi mafunde olimba a nyanja.

5 Mboni zanu zibvomerezeka ndithu;

Ciyero ciyenera nyumba yanu, Yehova, ku nthawi za muyaya.