Onse a pansi pano ndi am’mwamba omwe alemekeze Mulungu
1 Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano;
Myimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.
2 Myimbireni Yehova, lemekezani dzina lace;
Lalikirani cipulumutso cace tsiku ndi tsiku.
3 Fotokozerani ulemerero wace mwa amitundu;
Zodabwiza zace mwa mitundu yonse ya anthu.
4 Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;
Ayenera amuope koposa milungu yonse.
5 Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano:
Koma Yehova analenga zakumwamba.
6 Pamaso pace pali ulemu ndi ukulu:
M’malo opatulika mwace muli mphamvu ndi zocititsa kaso.
7 Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu,
Mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu,
8 Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lace;
Bwerani naco copereka, ndipo fikani ku mabwalo ace.
9 Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa:
Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi.
10 Nenani mwa amitundu, Yehova acita ufumu;
Dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;
Adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
11 Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;
Nyanja ibume mwa kudzala kwace:
12 Munda ukondwerere ndi zonse ziri m’mwemo;
Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera;
13 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza;
Pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi:
Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi cilungamo,
Ndi mitundu ya anthu ndi coonadi.