Ulemerero wa ufumu wa Mulungu
1 Yehova acita ufumu; dziko lapansi likondwere;
Zisumbu zambiri zikondwerere.
2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima;
Cilungamo ndi ciweruzo ndizo zolimbitsa mpando wacifumu wace.
3 Moto umtsogolera,
Nupsereza otsutsana naye pozungulirapo,
4 Mphezi zace zinaunikira dziko lokhalamo anthu;
Dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.
5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,
Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Kumwamba kulalikira cilungamo cace,
Ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wace.
7 Onse akutumikira fano losema,
Akudzitamandira nao mafano, acite manyazi:
Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.
8 Ziyoni anamva nakondwera,
Nasekerera ana akazi a Yuda;
Cifukwa ca maweruzo anu, Yehova.
9 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,
Ndinu wokwezeka kwakukuru pamwamba pa milungu yonse yina.
10 Inuokonda Yehova, danani naco coipa:
Iye asunga moyo wa okondedwa ace;
Awalanditsa m’manja mwa oipa.
11 Kuunika kufesekera wolungama, Ndi cikondwerero oongoka mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;
Ndipo yamikani pokumbukila ciyero cace.