Masalmo 98

Alemekeze Mulungu pa cifundo ndi coonadi cao

Sa1mo.

1 Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano;

Popeza anacita zodabwiza:

Dzanja lace lamanja, mkono wace woyera, zinamcitira cipulumutso,

2 Yehova anawadziwitsira cipulumutso cace;

Anaonetsera cilungamo cace pamaso pa amitundu.

3 Anakumbukila cifundo cace ndi cikhulupiriko cace ku nyumba ya Israyeli;

Malekezero onse a dziko lapansi anaona cipulumutso ca Mulungu wathu.

4 Pfuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;

Kuwitsani ndi kupfuulira mokondwera; inde, yimbirani zomlemekeza.

5 Myimbireni Yehova zomlemekeza ndizeze;

Ndi zeze ndi mau a salmo.

6 Pfuulani pamaso pa Mfumu Yehova,

Ndi mbetete ndi liu la lipenga,

7 Nyanja Ipfuule ndi kudzala kwace;

Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;

8 Mitsinje iombe manja;

Mapiri apfuule pamodzi mokondwera;

9 Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi;

Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi cilungamo,

Ndi mitundu ya anthu molunjika,