Mulungu wamkuru wacifundo alemekezedwe
1 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;
Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
2 Yehova ndiye wamkuru m’Ziyoni;
Ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3 Alemekeze dzina lanu lalikuru ndi loopsa;
Ili ndilo loyera.
4 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda ciweruzo;
Inu mukhazikitsa zolunjika,
Mucita ciweruzo ndi cilungamo m’Yakobo.
5 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,
Ndipo padirani poponderapo mapasa ace:
Iye ndiye Woyera.
6 Mwa ansembe ace muli Mose ndi Aroni,
Ndi Samueli mwa iwo akuitanira dzina lace;
Anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
7 Iye analankhula nao mumtambo woti njo:
Iwo anasunga mboni zace ndi malembawa anawapatsa,
8 Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:
Munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,
Mungakhale munabwezera cilango pa zocita zao.
9 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,
Ndipo gwadirani pa phiri lace loyera;
Pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.