Masalmo 100

Olengedwa ndi Mulungu amlemekeze

Salmo la Ciyamiko.

1 Pfuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi.

2 Tumikirani Yehova ndi cikondwerero:

Idzani pamaso pace ndi kumyimbira mokondwera,

3 Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu;

Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ace;

Ndife anthu ace ndi nkhosa za pabusa pace.

4 Lowani ku zipata zace ndi ciyamiko,

Ndi ku mabwalo ace ndi cilemekezo:

Myamikeni; lilemekezeni dzina lace.

5 Pakuti Yehova ndiye wabwino; cifundo cace cimamka muyaya;

Ndi cikhulupiriko cace ku mibadwo mibadwo.