Alemekeza Mulungu pa nchito zao zazikuru zokoma
1 Haleluya.
Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse,
Mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
2 Nchito za Yehova nzazikuru,
Zofunika ndi onse akukondwera nazo.
3 Cocita Iye nca ulemu, ndi ukuru:
Ndi cilungamo cace cikhalitsa kosatha.
4 Anacita cokumbukitsa zodabwiza zace;
Yehova ndiye wa cisomo ndi nsoni zokoma.
5 Anapatsa akumuopa Iye cakudya;
Adzakumbukila cipangano cace kosatha.
6 Anaonetsera anthu ace mphamvu ya nchito zace,
Pakuwapatsa colowa ca amitundu.
7 Nchito za manja ace ndizo caonadi ndi ciweruzo;
Malangizo ace onse ndiwo okhulupirika.
8 Acirikizika ku nthawi za nthawi,
Acitika m’coonadi ndi cilunjiko,
9 Anatumizira anthu ace cipulumutso;
Analamulira cipangano cace kosatha;
Dzina lace ndilo loyera ndi loopedwa.
10 Kumuopa Yehova ndiko ciyambi ca nzeru;
Onse akucita cotero ali naco cidziwitso cokoma;
Cilemekezo cace cikhalitsa kosatha.