Masalmo 112

Adalitsidwa akuopa Mulungu

1 Haleluya.

Wodala munthu wakuopa Yehova,

Wakukondwera kwambiri ndi malamulo ace,

2 Mbeu yace idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi;

Mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

3 M’nyumba mwace mudzakhala akatundu ndi cuma:

Ndi cilungamo cace cikhala cikhalire.

4 Kuupika kuturukira oongoka mtima mumdima;

Iye ndiye wacisomo; ndi wansoni ndi wolungama.

5 Wodala munthu wakudtira cifundo, nakongoletsa;

Adzalimbika nao mlandu wace poweruzidwa.

6 Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse:

Wolunguna adzakumbukika ku nthawi yosatha.

7 Sadzaopa mbiri yoipa;

Mtima wace ngwokhazikika, wakhulupirira Yehova.

8 Mtima wace ngwocirikizika, sadzacita mantha,

Kufikira ataona cofuna iye pa iwo omsautsa.

9 Anagawagawa, anapatsa aumphawi;

Cilungamo cace cikhalitsa kosatha;

Nyanga yace idzakwezeka ndi ulemu.

10 Woipa adzaziona, nadzapsa mtima;

Adzakukuta mano, nadzasungunuka;

Cokhumba oipa cidzatayika.