Anthu onse alemekeze dzina la Mulungu wothandiza aumphawi
1 Haleluya;
Lemekezani, inu atumiki a Yehova;
Lemekezani dzina la Yehova,
2 Lodala dzina la Yehova.
Kuyambira tsopano kufikira kosatha.
3 Citurukire dzuwa kufikira kulowa kwace
Lilemekezedwe dzina la Yehova.
4 Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse,
Ulemerero wace pamwambamwamba.
5 Akunga Yehova Mulungu wathu ndani?
Amene akhala pamwamba patali,
6 Nadzicepetsa apenye
Zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi.
7 Amene autsa wosauka lrumcotsa kupfumbi,
Nakweza waumphawi kumcotsa kudzala.
8 Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu,
Pamodzi ndi akulu a anthu ace.
9 Asungitsa nyumba mkazi wosaonamwana,
Akhale mai wokondwera ndi ana.
Haleluya.