Alemekeze Mulungu pa cipulumutso cija ca m’Aigupto
1 M’mene Israyeli anaturuka ku Aigupto,
Nyumba ya Yakobo kwa anthu a cinenedwe cacilendo;
2 Yuda anakhala malo ace oyera, Israyeli ufumu wace.
3 Nyanjayo inaona, nithawa;
Yordano anabwerera m’mbuyo.
4 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo,
Timapiri ngati ana a nkhosa.
5 Unathawanji nawe, nyanja iwe?
Unabwerereranji m’mbuyo, Yordano iwe?
6 Munatumpha-tumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu?
Ngati ana a nkhosa, zitunda inu?
7 Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye,
Pamaso pa Mulungu wa Yakobo;
8 Amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi,
Nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.