Masalmo 118

Wa Salmo alemekeza Mulungu womlanditsa m’manja mwa adani

1 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;

Pakuti cifundo cace ncosatha.

2 Anene tsono Israyeli,

Kuti cifundo cace ncosatha.

3 Anene tsono nyumba ya Aroni,

Kuti cifundo cace ncosatha.

4 Anene tsono iwo akuopa Yehova,

Kuti cifundo cace ncosatha.

5 M’mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;

Anandiyankha Dandiika motakasuka Yehova.

6 Yehova ndi wanga; sindidzaopa;

Adzandicitanji munthu?

7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;

M’mwemo ndidzaona cofuna ine pa iwo akundida,

8 Kuthawira kwa Yehova nkokoma

Koposa kukhulupirira munthu.

9 Kuthawira kwa Yehova nkokoma

Koposa kukhulupirira akulu,

10 Amitundu onse adandizinga,

Zedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

11 Adandizinga, inde, adandizinga:

Indedi, m’dzinala Yehova ndidzawaduladula.

12 Adandizinga ngati njuci;

Anazima ngati moto waminga;

Indedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

13 Kundikankha anandikankha ndikadagwa;

Koma Yehova anandithandiza.

14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;

Ndipo anakhala cipulumutso canga.

15 M’mahema a olungama muli liu lakupfuula mokondwera ndi la cipulumutso:

16 Dzanja lamanja la Yehova licita mwamphamvu.

17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,

Ndipo ndidzafotokozera nchito za Yehova.

18 Kulanga anandilangadi Yehova:

Koma sanandipereka kuimfa ai.

19 Nditsegulireni zipata za cilungamo;

Ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.

20 Cipata ca Yehova ndi ici;

Olungama adzalowamo.

21 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,

Ndipo munakhala cipulumutso canga,

22 Mwala umene omangawo anaukana

Wakhala mutu wa pangondya.

23 Ici cidzera kwa Yehova;

Ncodabwiza ici pamaso pathu.

24 Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;

Tidzasekera ndi kukondwera m’mwemo.

25 Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;

Tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.

26 Wodala wakudzayo m’dzina la Yehova;

Takudalitsani kocokera m’nyumba ya Yehova.

27 Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;

Mangani nsembe ndi zingwe, ku nyanga za guwa la nsembe.

28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;

Ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.

29 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino,

Pakuti cifundo cace ncosatha.