Apempha Mulungu amlanditse pa Omnamiza
Nyimbo yokwerera.
1 Ndinapfuulira kwa Yehova mu msauko wanga,
Ndipo anandibvomereza,
2 Yehova, landitsani moyo wanga ku milomo ya mabodza,
Ndi ku lilime lonyenga.
3 Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji,
Lilime lonyenga iwe?
4 Mibvi yakuthwa ya ciphona.
Ndi makara tsanya.
5 Tsoka ine, kuti ndiri mlendo m’Meseke,
Kuti ndigonera m’mahema a Kedara!
6 Moyo wanga unakhalitsa nthawi
Pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere.
7 Ine ndikuti, Mtendere;
Koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.