Apempherera mtendere wa Yerusalemu
Nyimbo yokwerera: ya Davide.
1 Ndinakondwera m’mene ananena nane,
Tiyeni ku nyumba ya Yehova.
2 Mapazi athu alinkuima M’zipata zanu, Yerusalemu.
3 Yerusalemu anamangidwa
Ngati mudzi woundana bwino:
4 Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;
Akhale mboni ya kwa Israyeli,
Ayamike dzina la Yehova.
5 Pakuti pamenepo anaika mipando ya ciweruzo,
Mipando ya nyumba ya Davide.
6 Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;
Akukonda inu adzaona phindu.
7 M’linga mwako mukhale mtendere,
M’nyumba za mafumu mukhale phindu.
8 Cifukwa ca abale anga ndi mabwenzi anga,
Ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.
9 Cifukwa ca nyumba ya Yehova Mulungu wathu
Ndidzakufunira zokoma,