Masalmo 125

Okhulupirira Yehova akhazikika mtima

Nyimbo yokwerera.

1 Iwo akukhulupirira Yehova

Akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha,

2 Monga mapiri azinga Yerusalemu,

Momwemo Yehova azinga anthu ace,

Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

3 Pakuti ndodo yacifumu ya coipa siidzapumula pa gawo la olungama;

Kuti olungama asaturutse dzanja lao kucita cosalungama,

4 Citirani cokoma, Yehova, iwo okhala okoma;

Iwo okhala oongoka mumtima mwao.

5 Koma iwo akupatuka kutsata njira zao zokhotakhota,

Yehova adzawacotsa pamodzi ndi ocita zopanda pace.

Mtendere ukhale pa Israyeli.