Masalmo 126

Ayamikira mokondwerera kuti Mulungu anabweza ukapolo wao

Nyimbo yokwerera.

1 Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni,

Tinakhala ngati anthu akulota.

2 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka,

Ndi lilime lathu linapfuula mokondwera;

Pamenepo anati mwa amitundu,

Yehova anawacitira iwo zazikuru,

3 Yehova anaticitira ife zazikuru;

Potero tikhala okondwera.

4 Bwezani ukapolo wathu, Yehova,

Ngati mitsinje ya ku Mwera.

5 Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kupfuula mokondwera.

6 Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa;

Adzabweranso ndithu ndi kupfuula mokondwera, alikunyamula mitolo yace.